Mbuzi, Galu ndi Ng’ombe anali mabwenzi kwambili. Tsiku lina, anapita paulendo ndi galimoto.
Goat, Dog, and Cow
were great friends. One
day they went on a
journey in a taxi.
Pamene anafika pothela pa ulendo wao, mtekenya anawafunsa kuti alipile ndalama. Ng’ombe inalipila yake.
When they reached the
end of their journey, the
driver asked them to
pay their fares. Cow
paid her fare.
Galu analipila ndalama yopitililapo chifukwa analibe ndalama yoyenela.
Dog paid a bit extra,
because he did not
have the correct money.
Mtekenya anali pafupi kupatsa Galu chenji yake pamene mbuzi inathawa kopanda kulipila.
The driver was about to
give Dog his change
when Goat ran away
without paying
anything.
Mtekenya anakalipa kwambili. Anayenda popanda kupatsa Galu chenji yake.
The driver was very
annoyed. He drove
away without giving
Dog his change.
Ndiye cifukwa cake, ngakhale lelo lomwe, Galu amathamangila galimoto kuona mkati ndi kupeza mtekenya amene ali ndi chenji yake.
That is why, even
today, Dog runs
towards a car to peep
inside and find the
driver who owes him his
change.
Mbuzi imathawa ikamvela galimoto. Imaopa kuti angaimangidwe chifukwa siinalipile mtekenya.
Goat runs away from
the sound of a car. She
is afraid she will be
arrested for not paying
her fare.
Ndipo Ng’ombe siimaikako nzelu ngati galimoto ili kubwela. Ng’ombe imayenda pang’ono pang’ono cifukwa idziwa kuti inalipila ndalama mokwana.
And Cow is not
bothered when a car is
coming. Cow takes her
time crossing the road
because she knows she
paid her fare in full.