M’ngono wanga amacedwa kugona. Ndimauka m’mamawa cifukwa ndine wamkulu!
My little brother sleeps very late. I wake early, because I am great!
Ndine ndimalowetsa dzuwa.
I am the one who lets in the sun.
“Ndiwe nthanda yanga yam’mawa,” amatero amai.
“You’re my morning star,” says Ma.
Ndimasamba ndekha masiku onse, sindifunanso thandizo iriyonse.
I wash myself, I don’t need any help.
Ndingasambe ndi madzi odzidzira, ndi sopo wamtambo onunkhira.
I can cope with cold water and blue smelly soap.
Amai amandikumbutsa,”osayiwala kutsuka mano.” Ndimawayanka kuti “ine ai, sindingaiwale ai!”
Ma reminds, “Don’t forget teeth.” I reply, “Never, not me!”
Ndikasiriza kusamba, ndimapatsa moni agogo amuna ndi alongo a atate anga. Ndimawafunira tsiku labwino.
After washing, I greet Grandpa and Auntie, and wish them a good day.
Kenaka ndimabvala ndekha. “Ndine wamkulu tsopano amama,” ndimanena.
Then I dress myself, “I’m big now Ma,” I say.
Ndimanga mabatani komanso nthambo za nsapato ndekha.
I can close my buttons and buckle my shoes.
Ndimayesetsa kuti mbale wanga adziwe nkhani zonse za kusukulu.
And I make sure little brother knows all the school news.
Mukalasi ndimacita zonse zothekera munjira iriyonse.
In class I do my best in every way.
Ndimacita zabwino zonsezi tsiku ndi tsiku. Koma cimene ndikondetsetsa kwambiri ndi kusowera!
I do all these good things every day. But the thing I like most, is to play and play!