Download PDF
Back to stories list

Nkhuku ndi Nkhwazi Hen and Eagle

Written by Ann Nduku

Illustrated by Wiehan de Jager

Translated by Sitwe Benson Mkandawire

Read by Christine Mwanza

Language Nyanja

Level Level 3

Narrate full story The audio for this story is currently not available.


Panali-panali, nkhuku ndi nkhwazi anali abwenzi. Anakhala mumutendere ndi mbalame zina. Panalibe paiwo amene anali kuuluka.

Once upon a time, Hen and Eagle were friends. They lived in peace with all the other birds. None of them could fly.


Tsiku lina, kunali njala kudziko. Nkhwazi anali kuyenda kutali kukasaka cakudya. Anabwerako olema kwambiri. “Kufunikira kukhala njira ina yapafupi mumayendedwe” Nkhwazi inatero.

One day, there was famine in the land. Eagle had to walk very far to find food. She came back very tired. “There must be an easier way to travel!” said Eagle.


Mumawa mwace, nkhuku inali ndi ganizo labwino. Inayamba kutola nthenga za mbalane iriyonse yamene inagwa. “Tiyeni tisokere pamodzi nthenga zamene tiri nazo” inatero nkhuku. “Mwina ici cidzakhala capafupi kuyenda.”

After a good night’s sleep, Hen had a brilliant idea. She began collecting the fallen feathers from all their bird friends. “Let’s sew them together on top of our own feathers,” she said. “Perhaps that will make it easier to travel.”


Nkhwazi ndiye anali cabe ndi nsingano yotungira pamudzi, iye anayambirira kusoka. Anazipangira mapiko awiri abwino-bwino nakuuluka pamwamba pa nkhuku. Nkhuku inabweleka nsingano koma analema kutunga. Anasiya nsingano yosokeira pa kabati ndipo anayenda kukakonza cakudya ca ana ake ku khicini.

Eagle was the only one in the village with a needle, so she started sewing first. She made herself a pair of beautiful wings and flew high above Hen. Hen borrowed the needle but she soon got tired of sewing. She left the needle on the cupboard and went into the kitchen to prepare food for her children.


Mbalame zina zinaiona nkhwazi kuuluka. Zinafunsa nkhuku kuti iwabwereke nsingano kuti zipangire mapiko youlukira nao. Mosacedwa, kunali mbalame zambiri kuuluka mumwamba.

But the other birds had seen Eagle flying away. They asked Hen to lend them the needle to make wings for themselves too. Soon there were birds flying all over the sky.


Pamene mbalame yomalizira inabweza nsingano yosokelira, nkhuku panalibe. Ana a nkhuku anatenga nsingano nakuyamba kusowera nayo. Pamene analema kusowera, anasiya nsingano ija mumcenga.

When the last bird returned the borrowed needle, Hen was not there. So her children took the needle and started playing with it. When they got tired of the game, they left the needle in the sand.


Mumazulo, nkhwazi anabwerera. Anapempha nsingano kuti asokere nthenga zimene zinasokomoka paulendo. Nkhuku inasakira nsingano pakabati, mophikira, ndi panja pa nyumba. Koma nsingano sinapezeke.

Later that afternoon, Eagle returned. She asked for the needle to fix some feathers that had loosened on her journey. Hen looked on the cupboard. She looked in the kitchen. She looked in the yard. But the needle was nowhere to be found.


“Ndipatseni tsiku limodzi” Nkhuku inapempha nkhwazi. “Kuti mukakonze phiko lanu ndikuulukanso kukasakira cakudya.” “Tsiku limodzi cabe” Nkhwazi anatero. “Ngati siupeza nsingano, uzandipatsa mwana wako m’modzi kukhala malipiro.”

“Just give me a day,” Hen begged Eagle. “Then you can fix your wing and fly away to get food again.” “Just one more day,” said Eagle. “If you can’t find the needle, you’ll have to give me one of your chicks as payment.”


Pamene nkhwazi inabwela tsiku lotsatirapo, anapeza nkhuku asakirabe mumcenga, koma nsingano sanaipeze. Nkhwazi anauluka mwamsanga ndikugwira kamwana ka nkhuku kamodzi. Anapita nako kutali. Kucokera nthwiyo, nkhwazi ikaonekela cabe, iona nkhuku isakira nyeleti mumicenga.

When Eagle came the next day, she found Hen scratching in the sand, but no needle. So Eagle flew down very fast and caught one of the chicks. She carried it away. Forever after that, whenever Eagle appears, she finds Hen scratching in the sand for the needle.


Ngati mthunzi wa phiko ya nkhwazi waonekela kucoka kumwamba, Nkhuku icenjeza ana ake. “Cokani poonekela.” Ndiponso iwo akuyankha, “Sindife oputsa, tizathamanga.”

As the shadow of Eagle’s wing falls on the ground, Hen warns her chicks. “Get out of the bare and dry land.” And they respond: “We are not fools. We will run.”


Written by: Ann Nduku
Illustrated by: Wiehan de Jager
Translated by: Sitwe Benson Mkandawire
Read by: Christine Mwanza
Language: Nyanja
Level: Level 3
Source: Hen and Eagle from African Storybook
Creative Commons License
This work is licensed under a Creative Commons Attribution 3.0 International License.
Options
Back to stories list Download PDF