Andiswa anapenyelela anyamata akusowela mpila. Analakalaka kusowela nao. Anapempha atsogoleli amasowela ngati angaloledwe kusowela nao.
Andiswa watched the boys play soccer. She wished that she could join them. She asked the coach if she can practise with them.
Atsogoleli amasowela anaika manja yao muciuno cake. “Pano pasukulu, anyamata okha ndiye ololedwa kusowela mpila,” anatelo.
The coach put his hands on his hips. “At this school, only boys are allowed to play soccer,” he said.
Anyamata anamuuza kuti akasowele masowela ampila wamanja. Ananena kuti mpila wamanja ndi wa atsikana ndipo mpila wa miyendo ndi wa anyamata. Andiswa anakhumudwa.
The boys told her to go play netball. They said that netball is for girls and soccer is for boys. Andiswa was upset.
Tsiku lotsatila, sukulu inakhala ndi masowela akulu ampila. Asogoleli ampila anadankhawa cifukwa katswili wao wampila anadwala ndiponso sanakwanitse kusewela mpila.
The next day, the school had a big soccer match. The coach was worried because his best player was sick and could not play.
Andiswa anathamagila kwa atsogoleli amasowela ampila kupapata kuti amuvomeleze asowele. Musogoleli sanadziwe cocita. Anaganiza kuti Andiswa angasowele mpila.
Andiswa ran to the coach and begged him to let her to play. The coach was not sure what to do. Then he decided that Andiswa could join the team.
Masowela anali obvuta. Kulibe anagoletsa kufika pakati panthawi yamasewela.
The game was tough. Nobody had scored a goal by half time.
Munthawi yaciwili yampila mnyamata m’modzi anapatsila Andiswa mpila. Mtsikana anathamanga mwamsanga kupita kugolo. Anamenya mpila mwamphamvu ndikugoletsa cigoli.
During the second half of the match one of the boys passed the ball to Andiswa. She moved very fast towards the goal post. She kicked the ball hard and scored a goal.
Anthu openyelela mpila anakondwela kwambili. Kucokela pa tsiku limenelo, atsikana analoledwa kusewela masowela ampila pa sukuklu.
The crowd went wild with joy. Since that day, girls were also allowed to play soccer at the school.