Back to stories list

Zomwe Mulongo wa Vusi Ananena What Vusi's sister said

Written by Nina Orange

Illustrated by Wiehan de Jager

Translated by Sitwe Benson Mkandawire

Read by Christine Mwanza

Language Nyanja

Level Level 4

Narrate full story The audio for this story is currently not available.


M’mawa mulimonse agogo a Vusi amamuitana, “Vusi, ndikupempha kuti upeleke dzilali ku makolo ako. Afuna kupanga keke yaikulu yapa cikwati ca mulongo wako.”

Early one morning Vusi’s granny called him, “Vusi, please take this egg to your parents. They want to make a large cake for your sister’s wedding.”


Mnjila poyenda kumakolo, Vusi anakumana ndi anyamata awili amene anali kuthyola zipatso. Mnyamata umodzi anatenga dzila lomwe linali ndi Vusi ndikuiponyela pamtengo. Dzila inaphwanyika.

On his way to his parents, Vusi met two boys picking fruit. One boy grabbed the egg from Vusi and shot it at a tree. The egg broke.


“Kodi ndi ciani cimene wacita?” Vusi analila. Dzila lija linali la keke. Kekeyo inali yapacikwati ca mlongo wanga. Kodi mlonga wanga azanena ciani ngati palibe keke pacikwati?”

“What have you done?” cried Vusi. “That egg was for a cake. The cake was for my sister’s wedding. What will my sister say if there is no wedding cake?”


Anyamata anapepesa ponena Vusi. “Sitingathandizile pa nkhani ya keke, koma tenga kumtengo aka koyendela ukapatse mlongo wako,” umodzi mwa iwo anatelo. Vusi anapitiliza ndi ulendo wake.

The boys were sorry for teasing Vusi. “We can’t help with the cake, but here is a walking stick for your sister,” said one. Vusi continued on his journey.


Mnjila anakumananso ndi amuna awili amene anali kumanga nyumba. Kodi tingasewenzetse ako kamtengo kolimba? Mwamuna umodzi anafunsa. Koma kamtengo sikanali kolimba ndiponso kanathyoka.

Along the way he met two men building a house. “Can we use that strong stick?” asked one. But the stick was not strong enough for building, and it broke.


“Kodi ndi ciani cimene mwacita?” Vusi analila. Ako kamtengo kanali mphaso ya mlonga wanga. Anthu otenga zipatso anandipatsa cifukwa anaphwanya dzila la keke. Keke inali ya cikwati ca mlongo wanga. Tsopano kulibe dzila, kulibe keke, ndiponso kulibe mphaso. Kodi mlonga wanga adzanena ciani?

“What have you done?” cried Vusi. “That stick was a gift for my sister. The fruit pickers gave me the stick because they broke the egg for the cake. The cake was for my sister’s wedding. Now there is no egg, no cake, and no gift. What will my sister say?”


Omanga nyumba anapepesa pothyola kamtengo. “Sitingathandizile pa nkhani ya keke, koma tenga mtolo wa udzu ukapatse mlongo wako,” umodzi pa omanga anatelo. Vusi anapitiliza ndi ulendo wake.

The builders were sorry for breaking the stick. “We can’t help with the cake, but here is some thatch for your sister,” said one. And so Vusi continued on his journey.


Poyenda mnjila, Vusi anakumana ndi mlimi ndi ng’ombe. “Mtolo wa udzu waoneka bwino, ungandipatseko kang’ono? Ng’ombe inafunsa. Mtolo wa udzu unakoma kwimbili ndiponso, ngombe inadya onse.

Along the way, Vusi met a farmer and a cow. “What delicious thatch, can I have a nibble?” asked the cow. But the thatch was so tasty that the cow ate it all!


“Kodi ndi ciani cimene wacita?” Vusi analila. Uyo mtolo unali wa udzu unali mphaso ya mlonga wanga. Anthu omanga manyumba anandipatsa cifukwa anathyola kamtengo kamene anandipatsa othyola zipatso. Othyola zipatso anandipatsa kamtengo cifukwa anaphwanya dzila la keke la mlongo wanga. Keke inali ya cikwati ca mlongo wanga. Tsopano kulibe dzila, kulibe keke, ndiponso kulibe mphatso. Mlonga wanga adzanena cani?

“What have you done?” cried Vusi. “That thatch was a gift for my sister. The builders gave me the thatch because they broke the stick from the fruit pickers. The fruit pickers gave me the stick because they broke the egg for my sister’s cake. The cake was for my sister’s wedding. Now there is no egg, no cake, and no gift. What will my sister say?”


Ng’ombe inapepesa pokudya mtolo. Mlimi anamupatsa ng’ombe kukhala mphatso ya mlongo wa Vusi. Vusi anapiliza ulendo wake.

The cow was sorry she was greedy. The farmer agreed that the cow could go with Vusi as a gift for his sister. And so Vusi carried on.


Koma ng’ombe inathawila kumwine wake pa cakudya ca m’madzulo. Vusi anasowa paulendo wake. Anafika mocedwa kwambili pacikwati ca mlongo wake. Alendo anayamba kale kudya pacikwati.

But the cow ran back to the farmer at supper time. And Vusi got lost on his journey. He arrived very late for his sister’s wedding. The guests were already eating.


“Kodi ndidzacita ciani?” Vusi analila. Ngo’mbe imene yathawa inali mphatso, m’malo mwa mtolo wa udzu umene anandipatsa omanga manyumba. Anthu omanga manyumba anandipatsa cifukwa anathyola kamtengo kamene anandipatsa othyola zipatso. Othyola zipatso anandipatsa kamtengo cifukwa anaphanya dzila la keke la mlongo wanga. Keke inali ya cikwati ca mlongo wanga. Tsopano kulibe dzila, kulibe keke, ndiponso kulibe mphatso.

“What shall I do?” cried Vusi. “The cow that ran away was a gift, in return for the thatch the builders gave me. The builders gave me the thatch because they broke the stick from the fruit pickers. The fruit pickers gave me the stick because they broke the egg for the cake. The cake was for the wedding. Now there is no egg, no cake, and no gift.”


Mlongo wa Vusi anaganiza kwambili ndiponso anati, “Vusi m’bale wanga, sindifuna za mphatso. Sindifunanso keke! Tilitonse pano pamodzi, ndiye camene candikondweletsa. Tsopano vala zovala zabwino mwakuti tisangalale lelo. Izo ndiye zamene anacita Vusi.

Vusi’s sister thought for a while, then she said, “Vusi my brother, I don’t really care about gifts. I don’t even care about the cake! We are all here together, I am happy. Now put on your smart clothes and let’s celebrate this day!” And so that’s what Vusi did.


Written by: Nina Orange
Illustrated by: Wiehan de Jager
Translated by: Sitwe Benson Mkandawire
Read by: Christine Mwanza
Language: Nyanja
Level: Level 4
Source: What Vusi's sister said from African Storybook
Creative Commons License
This work is licensed under a Creative Commons Attribution 3.0 International License.
Options
Back to stories list Download PDF