Tsiku lina, amai anatenga zipatso zambiri.
One day, mama got a lot of fruit.
“Ndipotani tingakhale ndi zipatso?” Tifunsa. “Tidzadya zipatso usiku walero” Anatero amai.
“When can we have some fruit?” we ask.
“We will have the fruit tonight,” says mama.
M’bale wanga Rahim ndi ozikonda. Alawa zipatso zonse. Adya ziphaso zambiri.
My brother Rahim is greedy. He tastes all the fruit. He eats a lot of it.
“Onani zimene Rahim anacita!” Anafuula m’bale wanga wamg’ono. “Rahim ndiwamakani ndiponso ozikonda” Nditero.
“Look at what Rahim did!” shouts my little brother.
“Rahim is naughty and selfish,” I say.
Amai ndiokalipa cifukwa ca Rahim.
Mother is angry with Rahim.
Naifenso ndife okwiya cifukwa ca Rahim. Koma Rahim sapepesa.
We are also angry with Rahim. But Rahim is not sorry.
“Kodi simuzamupatsa cirango?” Afunsa m’bale wamng’ono.
“Aren’t you going to punish Rahim?” asks little brother.
“Rahim, posacedwa apa, uzacita cisoni,” amucenjeza amai.
“Rahim, soon you will be sorry,” warns mama.
Rahim wayamba kumva kudwala.
Rahim starts to feel sick.
“M’mimba mwanga mwayamba kuwawa” anong’oza Rahim.
“My tummy is so sore,” whispers Rahim.
Amai anadziwa kuti izi zidzacitika. Cipatso cimupatsa cirango Rahim!
Mama knew this would happen. The fruit is punishing Rahim!
Pambuyo pake, Rahim apepesa kwa ife. “Sindidzakhalanso wazikonda tere,”. Alonjeza. Ndipo timukhulupirira tonse.
Later, Rahim says sorry to us. “I will never be so greedy again,” he promises.
And we all believe him.